Tingoyenera kukhaladi mavenda

Mwina tilembe anyamata ogulitsa nsapato kuti agulitse Software yathu

This article is written in Chichewa. I wanted to try something different. Here goes nothing

Mawu oti venda nthawi zambiri amatikumbutsa anyamata ndi amayi a mtawuni kapena kumsika omwe amagulitsa zinthu zosiyanasiyana monga nsapato, katundu wa magetsi ndi zina zambiri. Mavenda timawaona mosiyanabe ndi anthu a bizinesi zokhazikika. Koma tikabwela ku nkhani zokhuza Software, mawu okuti Software Vendor amatipatsa malingaliro a makampani aakulu monga Microsoft, ndi Oracle. Koteleko Software Vendor amakhala wolemekezeka ndithu.

Mkulingalira kwanga, ndikuona ngati mavenda "wambawa" akhonzabe kutiphunzitsa mmene tingapangire kuti nafe tidzafike pa mlingo wa makampani monga Microsoft ndi kumatchedwanso Software Vendor. Tiyeni tiunikile makhalidwe amavenda:

  1. Venda samaopa - nthawi zambiri venda amakhala wolimba mtima ndipo samaopa kutsatsa malonda ake. Venda wamanyazi sangagulitse kanthu. Venda amatha kutsatira munthu kamtunda akuyesera kumutsatsa malonda ake.

  2. Venda samachita manyazi kuonetsa malonda ake - munthu poti ufike pogula zinthu kwa venda, umakhala kuti malondawo waaona ndi maso, penanso nkuyesa komwe ngati chili chovala kapena nsapato. Venda saopa kuonetsa malonda ake ndipo amati "Kuyesa ndi ulere".

  3. Venda amatha kuyendamtunda kuti agulitse - mavenda ena amatha kuyenda mtunda wautali, kutiakapeze makasitomala. Izi si zachilendo ngati munaonapo anyamata ogulitsa madzi kapena mazira. Amatha kuyenda kutali ndi komwe achokela wapansi cholinga agulitse.

  4. Venda amayesa zida - Mavenda ambiri ndi ochenjera, ndipo amakonda kuyesa zida makamaka pa nkhani ya mitengo. Mavenda ambiri amangotchula mtengo wawo nadikira kuti munthu unenerere. Akatelo amakhala kuti awonjezerapo pa mtengo omwe anaodera katunduyo, ndipo akufuna kuwinapo. Ngati umatha kunenerera, udzaona kuti venda uja amatha kusitsa mtengo kwambiri kuchoka pomwe anayambira.

    Ineyo nnagulapo lamba mu dera la Lilongwe pa mtengo wa 2 sauzande, koma venda anandigulitsayo adayambira pa 12 sauzande. Sikuti ndimatha kunenelera, koma zinango chitika kuti amafunisitsa kuti apeze ndalama. Tikatelo tiwone mdemanga ina

  5. Venda ntchito yake ndi kugulitsa - venda amafuna kugulitsa, akapanda kugulitsa zimakhala kuti zake sizinayende. Ndipo nthawi zambiri tsiku likamatha mumaona ma venda ena amatha kugulitsa zinthu pa mtengo wozizira, cholinga chawo chimakhala choti agulitse basi. Za mawa aziona mawa lo. Khalidwe limeneli ili ndi ubwino ndi kuyipa kwake, koma chachikulu ndichoti mtima ofuna kugulitsa tsiku limenelo ndi omwe umapangitsa venda kuti alimbikire ndipo apeze njira ndi ma kasitomala.